Malawi Broadcasting Corporation
Local News Nkhani

MPUNGWEPUNGWE KUNYUMBA YAMALAMULO

Kuli mpungwepungwe ku nyumba ya malamulo pomwe zokambirana kunyumbayi zayamba ndipo a Kondwani Nankhumwa komanso  a Mary Navicha  anaimilira ngati mtsogoleri wa zipani zotsutsa.

Awiriwa anaimilira Sipikala wanyumbayi atafunsa kuti Otsutsa boma ayankhepo pa zomwe anakambirana ku komiti ya atsogoleri oyendetsa zokambirana za nyumba yamalamulo.

Kusamvana kunabuka mnyumbayi  pomwe Sipikala wanyumbayi a Catherine Gotani Hara anavomereza a Kondwani Nankhumwa ngati mtsogoleri wa otsutsa ponena kuti malingana ndi chiletso cha khothi Pakadali pano a Mary Navicha sangaimilire mbali yotsutsayi komanso ku sanali nawo pazokambiranazi.

Apa mpomwe akumbali yotsutsa a chipani cha DPP anaima kutsutsana ndi gamulo la sipika.

A Gotani Hara alamula a Navicha ndi a Nankhumwa kuti akhale pansi kutengera ndi malamulo a mnyumbayi.

Pakadali pano zokambira nyumba yi aziimitsa kaye kwa mphindi khumi.

 

Wolemba: Olive Phiri ndi  Beatrice Mwape

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MUSALOLE ANA KUCHITA JUGA – MAGLA

MBC Online

Bungwe lathandiza maanja 20,000 kuthana ndi njala

Doreen Sonani

FAM hands 100 footballs to SULOM

Nobert Jameson
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.