Bungwe la Malawi Revenue Authority (MRA) lati likwanitsa kutolera ndalama zokwana K2.18 trillion mu chaka cha boma cha 2023/2024 chimene chikutha kumapeto a mwezi uno.
Mkulu wa bungwe la MRA, a John Bizwick, anena izi lachitatu mumzinda wa Blantyre pa msonkhano wa atolankhani.
A Bizwick ati pakadali pano, bungweli latolera ndalama zokwana K2.002 trillion mu miyezi ya pakati pa April chaka chatha ndi February chaka chino ndipo pakutha mwezi uno, akhala atakwanitsa kutolera K2.18 trillion.
Poyamba pa chaka chaboma cha 2023/2024, boma linawuza MRA kuti itolere K2.11 trillion koma kumathero a chakachi boma linakweza ndalamayi ndi K70 billion powuza bungweli kuti litolere K2.18 trillion.