Bungwe la atsogoleri a mipingo la Evangelical Association of Malawi (EAM) lati a Malawi ayambe kupempherera mvula kutsatira kugwa kwa ng’amba.
Mlembi wa mkulu wa bungwe la EAM, abusa Francis Mkandawire, ati amene angathe kusala kudya achite chomwecho komanso anthu akhale akupemphera molimba ku nyumba kwawo, malo opembedzera ndi malo ogwira ntchito.
“Mulungu achiritse dziko lathu natipatsa mvula yokwanira ndi kutichotsera mavuto ambiri tikukumana nawo ngati dziko,” a Mkandawire anafotokoza.
M’mbuyomu, nthambi ya za nyengo inati kuyambira mwezi wa February mpakana mwezi wa April, chaka chino, mvula ikhala ikugwa mwa njomba m’madera ambiri m’dziko muno.
Olemba: Romeo Umali