Asodzi awiri afa panyanja ya Malawi mphenzi itawaomba, malinga ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi.
A Daudi ati ngoziyi yachitika mdera la mfumu Moto mdera la mfumu yaikulu Namabvi.
“Tamvetsedwa kuti asodziwa anali panyanja kugwira ntchito yawo monga mwamasiku onse koma mwadzidzi kunayamba mphepo ya mwera ndi mvula yamphamvu yophatikizana ndi mphenzi yomwe inaomba bwato lawo,” a Daudi anatero.
Iwo anatinso chifukwa cha mphamvu za nyetsi ya mphenziyo, asodziwo anagwera m’madzi ndipo matupi awo apezeka atatentheka kwambiri.