Alimi a ng’ombe za mkaka a ku Mangunda m’boma la Thyolo ati akuyembekeza kuti phindu la ulimi wawo lichuluka kaamba kakuti pa malowa ayikako magetsi a mphamvu ya dzuwa.
Izi zikudza pamene alimiwa alandira thandizo la ndalama zokwana K107 million kuchokera ku TRADE Programme, ndondomeko ya boma yothandiza alimi.
Msungichuma wa gulu la alimiwa, a Elias Piringu, wati magetsi akathima amataya mkaka okwana malita 4000 ndi chifukwa anapempha thandizo la magetsiwa komanso mapampu amadzi.