Msonkhano waukulu wa mpingo wa CCAP mu Sinodi ya Livingstonia anayamba awuyimitsa kaye moderator watsopano wa sinodiyi, m’busa Jairos Kamisa, atadzudzula akuluakulu a mpingowo ‘chifukwa chosokoneza zinthu’.
Iwo anadzudzula akuluakuluwo, kuphatikizapo mlembi wamkulu wa sinodiyi, m’busa William Tembo, kuti amalowelera mu nkhani zandale, komanso amayambitsa zinthu zogawanitsa mpingo ndikuchita ziganizo mosafunsa maganizo a Moderator.
Izi zinachititsa kuti m’busa Tembo akhetse misozi pamaso pagulu lonse limene linasonkhana mu tchalichi cha Embangweni ku Mzimba.
Mmodzi mwa akuluakulu opuma a mpingowo, m’busa Mezuwa Banda, anapempha moderator watsopanoyo kuti zokambiranazo aziyimitse kaye.
Olemba: Hassan Phiri