Nduna yofalitsa nkhani a Moses Kunkuyu yatsindika zakufunika koti aMalawi adziganiza mozama m’mene angamatukulire maanja awo, madera komanso dziko lonse ngati muja achitira akatswiri osewera mpira wa miyendo.
A Kunkuyu amayankhula izi ku Blantyre pamene amakhazikitsa chikho cha Tambala Super Cup ndipo anati nthawi yakwana yoti anthu adzikhala olimbikira kwambiri pa ntchito zonse zimene zingathandizire kupititsa patsogolo miyoyo yawo.
Iwo anadzudzulanso m’chitidwe wa atsogoleri ena a ndale amene amagwiritsa ntchito misonkhano komanso masamba a mchezo ndi kumafalitsa nkhani zabodza komanso zonyoza atsogoleri anzawo.
Pakadali pano, mfumu yayikulu Kuntaja yayamikira a Kunkuyu kaamba kokhazikitsa chikhochi chomwe adzipikisana matimu a m’mboma la Blantyre.