Boma mawa likhazikitsa mtukula pakhomo wa m’mizinda wa ndalama zokwana K15.7 billion.
Malinga ndi m’modzi mwa akuluakulu ku unduna wa zachuma, a Kate Langwe, mwambo okhazikitsa ndondomekoyi uchitika mawa pabwalo la Gymkana ku Zomba.
Kupyolera mu ndondomekoyi, mabanja okwana 105,000 alandira K150,000 banja lililonse.
Ndalamayi ithandiza mabanjawa kuti apeze chakudya mosavuta ndi kuthandiza kuti asabooke mnthumba pogula katundu kamba ka kukwera mtengo.
Pakadali pano, kalata yochokera kwa mlembi wamkulu mu unduna wazachuma, a Betchani Tchereni, yati kalembera wa anthu oti alandire ndalamayi wayambika mumizinda ya Blantyre, Lilongwe, Mzuzu ndi Zomba.
Ntchitoyi ikuchitika ndi thandizo lochokera ku World Bank, USAID, Iceland, Ireland, UK-FCDO, European Union komanso Norway.