Achinyamata a mdela la Mfumu yaikulu Mwirang’ombe ku Wovwe m’boma la Karonga awayamikira chifukwa chokhala ndi chidwi kuti aphunzire ntchito zaluso la manja mdelari.
Mfumu ya delari yanena izi pomwe achinyamata 90 alandira masatifiketi atatsiliza maphunziro awo, poonjezera kuti asonyeza chidwi chofuna kukhala nzika zodalirika.
Mkulu oyendetsa ntchito za bungwe lomwe limayang’anira maphunziro a ntchito zoterezi la TEVETA mchigawo chakumpoto a Joseph Chikopa auza MBC kuti ndizosangalatsa kuti nzika zamdela la Wovwe zikupindula zitagwirizana zoyitanitsa sukukuyi.
Wapampando wakhonsolo yaboma la Karonga a Bellium Msukwa anati ndiokondwa ndi sukuluyi ndipo anati aonetsetsa kuti apemphe khonsolo yawo kuti ikonze maofesi akale azaulimi a Wovwe omwe akungokhala kuti awakonzenso kuti akhale sukulu yokhazikika yantchito zaluso lamanja.
Olemba: Henry Haukeya