Mfumu yayikulu Ngokwe m’boma la Machinga yayamikira ntchito imene magulu ena, kuphatikizapo atsogoleri azipembedzo, akugwira pofikira mabanja amene akukumana ndi vuto la kusowa kwa chakudya.
Mfumuyi yanena izi pa bwalo la zamasewero la Ngokwe pamene utumiki wa Salvation for All Ministries International umapereka thandizo la chimanga ku mabanja okwana 2000 amene akukumana ndi vuto la kusowa kwa chakudya.
Malinga ndi mfumuyi, kwa zaka ziwiri anthu ochuluka mderali akhala akulephera kukolora chakudya chokwanira kaamba ka namondwe wa Freddy komanso ng’amba imene inaomba mdziko muno, zimene zachititsa kuti anthu ambiri asowe chakudya.
Mtsogoleri wa utumiki wa Salvation for All Ministries International, a Clifford Kawinga, wati kupatula ntchito yawo yolalikira uthenga wa Mulungu, utumiki wawo umazindikiranso kufunika kogwira ntchito zachifundo.
Iwo aperekanso thandizo la ndalama kwa mafumu, abusa azipembedzo zosiyanasiyana komanso ma Sheikh okhala mozungulira dera la mfumu yaikulu Ngokwe.
Olemba: Owen Mavula