Unduna wazaulimi wati nkofunika kugwirana manja polimbikitsa njira zamakono mu ulimi monga AI kuti ulimi upite patsogolo m’dziko muno.
Mkulu owona zantchito zaulimi mundunawu, a Pearson Jasi Soko, wayankhula izi ku Lilongwe ku msonkhano wamasiku atatu owunikira momwe angaphatikizire njira zamakonozi mu ulimi.
Mkumanowu ukuchitika pansi pantchito yoona zanjira zamakonozi pokweza ulimi ndi madyedwe abwino ya Digitally Enabled Resilience and Nutrition Policy Innovations DEPrin.
Mkulu yemwe akutsogolera ntchitoyi kuno Malawi, a Bennett Kankuzi, anati ndondomekoyi ithandiza alimi kupeza uthenga ofunikira mwansanga komanso kuchepetsa bvuto lakusowa Kwa uthenga oyenerera wazaulimi pogwiritsa ntchito njira zamakono.
Mmodzi mwa akuluakulu kubungwe la Farmers Union of Malawi, a Derrick Kapolo, ati ndizofunukira kuti alimi adzikhala nawo mmuntchito zomwe boma kaya mabungwe akukonza zokhudza ulimi kuti azidziwa za mbewu zoyenera kulima komanso zomwe dziko likusowekera.
Nondomeko ya DEPrin inayamba 2023 ndipo itha 2025 ndipo kuno ku Malawi akuyiyendetsa ndi a Malawi University of Science and Technology MUST mogwirizana ndi Akademiya2063 bungwe la mdziko la Rwanda, ndi thandizo slochekera GIZ.
Olemba: Emmanuel Chikonso