Adindo a khonsolo ya Mbelwa ati ntchito yomanga bwalo la masewero la Mzimba ikhala ikufika kumapeto pofika m’mwezi wa December chaka chino.
M’modzi mwa akulu akulu a khonsoloyi, a Allan Chitete, ati zambiri zofunikira pa bwalori zinatheka kale.
Bwalo limeneli ndi lokwana anthu 25, 000 ndipo lidzakhalanso ndi ma ofesi amene khonsoloyi idzidzachitira malonda.