Malawi Broadcasting Corporation
Agriculture Local Local News Nkhani

Mbeu zamakolo zikuchepa — Kafufukufuku

Kafukufuku yemwe ophunzira a sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR) achita mogwirizana ndi mabungwe amene amaona ntchito zosamalira chilengedwe m’dziko muno waonetsa kuti mbewu zambiri zimene makolo ankalima mu zaka zam’mbuyomo tsopano zikuchepa.

Izi zadziwika pa chionetsero cha mbewu chomwe mabungwe osiyanasiyana olimbikitsa zosamalira chilengedwe akonza kwa T/A Chamba m’boma la Machinga.

Ma bungwe a CARD ndi CADECOM ndi amene achita kafukufukuyu limodzi ndi ophunzira aku LUANAR.

Anastanzio Makhulula, yemwe ndi mmodzi mwa akuluakulu ku bungwe la CADECOM ku Zomba, wati bungweli likulimbikitsa alimi kuti adzigwiritsa ntchito mbewu za makolo chifukwa zili ndi kuthekera kochita bwino ngakhale nyengo itasintha.

Malinga ndi mkulu wa ntchito za malimidwe m’boma la Machinga, a Isaac Ali, yemwenso ndi mlendo olemekezeka pamwambowu, mbewu za makolo ndi zopilira kwambiri ku chilala kotero ndikofunika kuti alimi adzigwiritsa ntchito mbewu zimenezi.

Chionetserochi chikuyembekezeka kuchitikanso lachisanu pa 22 November 2024, m’boma la Balaka.

Olemba: Doreen Banda

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Local CSO wants Salima Sugar accounts unfrozen

Trust Ofesi

Mayi amangidwa poganiziridwa kuti wapha mwamuna wake

Romeo Umali

Ufa othandizira ovutika ndi njala wafika

Blessings Kanache
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.