Mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma ku Nyumba ya Malamulo, a Kondwani Nankhumwa, akana kulankhula mawu omaliza potsekera msonkhano wa aphunguwa, umene wakhala ukuchitika kwa sabata zisanu ndi zitatu.
Pamene Nyumba ya Malamulo ikumaliza msonkhano wake lero, Sipikala wa Nyumbayi, a Catherine Gotani Hara, anapereka mpata kwa mkulu wa chipani cha DPP a Mary Navitcha kuti alankhule mau awo omaliza pa msonkhanowu, ndipo atamaliza, a Catherine Gotani Hara anaperekanso mpata kwa mtsogoleri wa aphungu otsutsa boma mnyumbayi kuti nawo alankhulepo
Koma a Nankhumwa anakana kulankhula ponena kuti zomwe sipikalayu wachita polora a Navitcha kulankhula ndizosemphana ndi malamulo.