Nduna yoona za maboma aang’ono komanso umodzi ndi chikhalidwe, a Richard Chimwendo Banda, yati siyokhutitsidwa ndi m’mene gawo lina la msewu wa Chiwembe mu mzinda wa Blantyre awumangira.
Iyo imanena izi itayendera misewu yamadulira imene akuimanga mu mzindawu, ndipo iwo ati nkhaniyi asiyira akuluakulu oona za mamangidwewa.
Komabe, a Chimwendo Banda ati ndi okondwa kuti miseu yambiri yamangidwa bwino.
Olemba : Blessings Cheleuka