Boma, kudzera ku unduna wa za ulimi, lakhazikitsa njira zimene zithandizire kupititsa patsogolo ulimi wa thonje, ngati m’mene zidaliri kale, kudzera kutsegula misika yabwino komanso kukhazikitsa zipangizo zaulimi zotsika mtengo.
Nduna yoona za ulimi, a Sam Kawale, ndiyo yanena izi m’boma la Salima pamwambo otsekulira msika wa thonje wa chaka chino.
A Kawale ati mwazina, alimiwa akuyenera kuthandizidwanso kupeza ngongole mosavuta, ponena kuti dziko lino limayenera kupeza thonje lochuluka matani 50,000 pa chaka, zomwe padakali pano silikukwanitsa.
Chaka chino, thonje lili pa K900 pa Kilogramme, kusonyeza kukwera kusiyana ndi chaka chatha pamene linali pa K580 pa Kilogramme.