Katswiri wankhonya Limbani Masamba wabweza chipongwe chomwe adachitiridwa ndi Simeon Tcheta chaka chatha pomugonjetsa kudzera pa ma points pa nkhonya ya mtima bii yomwe inali pa Kamuzu Institute munzinda wa Lilongwe.
Anyamatawa anayamba molawana moto mu round yoyamba pomwe amachita ngati akungoseweretsana kenaka nkhonya inakolera mu round yachitatu pomwe zinayamba kubvumba
zibakera kuchokera mbali zonse ziwiri.
Masamba anadzambatuka kuyambira mu round yachisanu ndichimodzi kumupanikiza Tcheta ndimabindula omwe amalunjika kwambiri pakamwa ndi mnthiti, zomwe zinapangitsa kuti Tcheta ayambe kuoneka ofooka koma anaonetsa chamuna pomwe anakwanitsa kumaliza ma round onse khumi ndi awiri (12) kuti chigamulo apereke oweruza
(Judges).
Oweluzawa anamvana chimodzi pomwe onse anapereka nkhonyayi kwa Masamba kuti atenge lamba yemwe amasungidwa ndi Tcheta ndipo Masamba wati ndiokondwa kuti wabwenza chipongwe ndipo ndiokonzeka kuteteza lambayu kwa aliyense pomwe Tcheta wavomereza kugonjaku.
Pa Masewero ena aakulu, Yamikani Mtambo naye wagonjetsa Grey Chimkwapulo pa ma points pomwe Marriam Dick wathambitsa Fatima M’beka kudzera pa knock-out pa nkhonya ya atsikana.
Nkhonyayi inakonzedwa ndi New Dawn Boxing promotion yomwe mkulu wake ndi Mike Chimaliza.
By Foster Maulidi
#MBCDigital
#Manthu