Mabungwe olimbikitsa ufulu, YONECO ndi Standing Voices akuyenda m’misika m’madera osiyanasiyana kuphunzitsa anthu za kuipa kosala ndi kuchitira nkhanza anthu omwe ali ndi khungu la chialubino.
M’boma la Mulanje aphunzitsa anthu m’misika ya kwa Chonde, ku Limbuli ndi kwa Chinakakana kudzera mu zisudzo ndi magule.
Kwa Chinakanaka, mkulu oona zophunzitsa za ufulu ku bungwe la YONECO, a Titus Linzi ati anthu a chialubino akuphwanyiridwa ufulu mu njira zambiri zomwe anthu sadziwa kuti ndi kulakwira malamulo, ndipo kuti atha kulowa nazo kundende.
“Nkhanzazi ndi monga kuwakaniza kumanga ukwati, kuwatchula maina achipongwe monga napweri, pangolini, tomato wapachulu, zigoma. Palinso nkhanza zomwe zimaayamba chifukwa cha zikhulupiriro za bodza,” atero a Linzi.
Ntchitoyi akuitcha Ufulu Wanga Caravan Tours.