Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

MANEPO yayamikira Madam Chakwera polimbana ndi nkhanza za anthu achikulire

Mkulu wa bungwe la MANEPO, a Andrew Kavala, wayamikira mayi wa dziko lino, Madam Monica Chakwera, pa chidwi chawo choonetsetsa kuti achikulire m’dziko muno asamazunzidwe.

A Kavala anena izi pa bwalo la sukulu la Mwazisi m’boma la Rumphi pa phwando limene Madam Chakwera anakonzera amayi achikulire ngati mbali imodzi yokondwelera tsiku la anakubala.

Iwo ati, kudzera kwa Madam Chakwera, akutha kutsatira nkhani zochitira nkhanza anthu achikulire zimene amalandira ndi kuthana nazo.

A Kavala anati ndi okondwa kuti dziko lino liri ndi malamulo atsopano othandizira kuthana ndi nkhaza zimene achikulire amalandira.

Iwo ayamikiranso boma pa chikonzero chake chakuti kuyambira chaka cha mawa, achikulire 150,000 m’dziko muno adzilandira K18,000 yoti iwathandizire kusintha miyoyo yawo.

Apa iwo ati ntchito yosamalira achikulire ndi ya aliyense ndipo apempha achinyamata kuti agwirane manja poteteza achikulire m’dziko muno.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

World Bank yaonetsa chikhulupiliro ku boma la Malawi

MBC Online

MBC yasintha matchanelo pa DSTV, GOTV

Beatrice Mwape

‘Boma lithandiza onse’

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.