Boma lati lithana ndi mavuto amene akubwezeretsa m’mbuyo ntchito yopereka maphunziro a chitukuko amene ankawatcha kuti ‘a Kwacha’ kalero.
Nduna yoona kuti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, a Jean Sendeza, ati ena mwa mavutowa ndi kusowa zipangizo zophunzilira ndi kuphunzitsira komanso ndalama zolipilira aphunzitsi kuti anthu ambiri aphunzire kulemba, kuwerenga ndi kuwerengera.
Iwo amayankhula izi loweruka pa bwalo la sukulu ya Katelera m’boma la Salima pa mwambo okumbukira tsiku lolimbikitsa kulemba, kuwerenga ndi kuwerengera.
Iwo anati ndizofunikanso kuti maphunzirowa adzikhala m’chiyankhulo chimene anthu amayankhula malinga ndi dera lomwe akukhala chifukwa zithandiza anthu kuti adziphunzira ndi kumvetsa zinthu mwa nsanga.
Mwambowu uli pansi pa mutu okuti ‘kupititsa patsogolo maphunziro m’ziyankhulo zosiyanasiyana, chiyambi chomvetsetsana ndi mtendere okhazikika’.