Malawi Broadcasting Corporation
Development Education Local Local News Nkhani

Madam Chakwera ayamikira Press Trust potukula maphunziro

Mayi wa pfuko lino, Madam Monica Chakwera, athokoza bungwe la Press Trust pochirimika pa ntchito zotukula maphunziro m’dziko muno.
Madam Chakwera anena izi ku Chiyola mdera la Mwazisi m’boma la Rumphi pamene amatsegulira sukulu ya sekondale yoyendera ya Chiyola imene bungwe la Press Trust lamanga.
Iwo anayamikiranso bungweli pomanga sukulu zambiri m’dziko muno komanso malo ogonenera atsikana zimene ati zikutukula maphunziro.
Madam Chakwera ati kuchuluka Kwa chiwerengero cha anthu mdziko muno kwaonjezeranso vuto la kusowa kwa malo abwino ophunzirira m’sukulu zosiyanasiyana zimene ati boma silingathe kumanga pa kamodzi.
Mayi wa pfukoyi analimbikitsanso atsikana kuti asathamangire banja koma m’malo mwake aphunzire kuti adzakhale odzidalira pawokha komanso agwiritse ntchito mwayi wa sukuluyi kuti akonze tsogolo lawo.

Related posts

Chithumba Bridge connects communities to amenities in Mchinji

Rabson Kondowe

SULOM IN CLUBS’ FUNDRAISING DINNER

Rabson Kondowe

Salima Sugar makes K2.4 billion profit

Yamikani Simtowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.