Apolisi ku Limbe munzinda wa Blantyre akusunga mwana amene akuti makolo ake anamusiya pa golosale ina kwa Manje.
Ofalitsankhani pa Polisi ya Limbe, a Aubrey Singanyama, ati mwanayu dzina lake ndi Beatrice ndipo ndi wa mkazi komanso akuganizira kuti atha kukhala ndi zaka zapakati pa ziwiri kapena zitatu.
A Singanyama ati anthu amene akumudziwa mwanayu apite ku polisiyi mwamsanga kapena akauze a polisi amene ali nawo pafupi.