Bungwe la Mulakho wa a Lhomwe lati ndi lodabwa ndi mafumu ena omwe sakumvetsa zakusankha kwa mfumu yatsopano ya a Lhomwe Paramount Chief Kaduya.
Wapampando wa bungwe-li, a Muchanakwaye Mpuluka alankhula izi pamene mafumu ena atatu anauza olembankhani lachisanu lapitali kuti sakugwirizana ndi m’mene asankhila mfumu yatsopanoyi.
Koma a Mpuluka ati anthu-wa anali nawo pazokambirana ndipo onse anagwirizana zosankha a Kaduya ngati mfumu yawo.
Iwo adaonjezeranso kumema ma membala a bungwe lawo kuti apewe kumvera anthu andale amene akufuna kuwagawanitsa.
Lachitatu lapitali, mtsogoleli wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera adavomereza dzina la a Kaduya kuti ikhale mfumu.
Kusankha-ku kunali kukhazikitsa mfumu patadutsa zaka zoposa zisanu, potsatira imfa ya mfumu yaikulu Ngolongoliwa.
Olemba: Blessings Kanache