Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

Oyimbira mpira wamiyendo awapempha kuti agwire ntchito mwaukadaulo

Chinthuzi : Football Association of Malawi

Anthu wokonda masewero a mpira wamiyendo m’dziko muno atsindika zakufunika koti oyimbira masewerowa agwire ntchito yawo mwaukadaulo pofuna kuti mpikisano wa TNM Super League  wa chaka chino ukhale wapamwamba.

Mwa zina, anthuwa apempha woyimbirawa kuti asamawonetse kukondera timu iliyonse pomwe masewero akuchitika.

Popereka maganizo awo mu programme ya The Pot pa MBC, ambiri mwa anthuwa ati zakhala zili zodandaulitsa pomwe ena mwa oyimbirawa akhala akumalephera kupereka ziganizo zoyenera pa masewero ena, zomwenso zikumasokoneza mipikisano monga zinaliri chaka chatha.

Mpikisano wa TNM Super League uyambika kumapeto a sabata ino.

Timu FCB Nyasa Big Bullets, yomwe idali akatswiri a mpikisanowu chaka chapitachi, yagonjetsa timu ya Silver Strikers loweruka lapitali ndikutenganso chikho cha Charity Shield chomwe matimu amalimbirana kumayambiliro a a ligi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Police IG receives FDH Cup from Blue Eagles

Foster Maulidi

ESCOM builds 29 modern houses for Neno and Mwanza communities

MBC Online

Apalasa kuchoka Lilongwe mpaka Blantyre pofuna kutolera K100 million

Emmanuel Chikonso
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.