Chipatala cha Queen Elizabeth (QECH) munzinda wa Blantyre chati tsopano makina ake atatu mwa asanu othandiza anthu amene ali ndi vuto la impsyo ayamba kugwira ntchito.
Mmodzi mwa akuluakulu pa chipatalachi, Dr William Peno, anena izi pamene wachiwiri kwa nduna yoona za umoyo, a Noah Chimpeni, anakayendera zipinda zimene amasamalirako anthuwo.
Dr Peno ati kuoonongeka kwa makinawo kunachititsa kuti odwala ena adziwatumiza ku chipatala cha Kamuzu Central munzinda wa Lilongwe.
Iwo anati izi zimachititsa kuti adziwononga ndalama zochuluka zedi chifukwa chipatala cha QECH chimalandira anthu pafupifupi makumi awiri pa sabata omwe amakhala ndi vuto la impsyo.
Pakadali pano, a Dr Peno ati akuyembekezera kuti makina enawo ayambanso kugwira ntchito pamathero a sabata ino kaamba kakuti akuwakonza.
Masiku angapo apitawo, makinawa anasiya kugwira ntchito ndipo a Chimpeni atayendera zipindazo m’mbuyomu adalonjeza kuti boma lilowelerapo.