Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Mafumu apempha boma, mabungwe athandize Zoe Foundation

Mafumu apempha boma ndi mabungwe kuti athandize malo osamalira ana amasiye a Zoe Foundation komanso Temwani Chilenga, mtsikana amene akusamalira ana amasiye okwana 92 m’dera la mfumu yaikulu Kabudula.

Mfumu yaing’ono Njati yanena izi pomwe bungwe la Old Mutual limapereka thandizo la ndalama zokwana K5 million zoti zithandizire pantchito yosamala anawa.

Mfumuyi yati Zoe Foundation yathandiza kwambiri mderali, maka kwa ana amene anasiya sukulu m’mbuyomu kaamba kamavuto azachuma.

“Mtsikanayu akutithandiza kwambiri ndichifukwa tikupempha kuboma komanso mabungwe, pano palibe madzi komanso magetsi, moti ana amavutika Mjigo ukaonongeka” anatero a mfumu a Njati.

M’mawu ake, Chilenga anati akulimbikira ulimi komanso malonda ang’onoang’ono kuti apeze thandizo losamalira anawo.

Mkulu wa Old Mutual ku Malawi, a Roy Punungwe, ati apereka thandizoli ngati njira imodzi yosangalalira kuti bungwe lawo lakwanitsa zaka 70 likutumikira a Malawi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mipingo ithokoza okumba manda ku Area 18

MBC Online

Takhumudwa posawasankha a Navicha – NGOGCN

MBC Online

Ulendo wotsiriza wa Dr Chilima wayambika kupita ku Nsipe

Mayeso Chikhadzula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.