Malawi Broadcasting Corporation
Crime Nkhani

M’busa wapereka mimba kwa mtsikana atamunamiza kuti amuchiritsa matenda

Apolisi ku Mulanje amanga m’busa wina, Steven Zambia, wazaka 38, pomuganizira kuti wakhala akugwililira mtsikana wazaka 15 kuchokera mwezi wa February mpaka June chaka chino pomunamiza kuti amuchiritsa matenda a khunyu omwe akudwala.

Mneneri wa apolisi ku Mulanje a Innocent Moses ati makolo a mtsikanayo akhala akuyitana anthu opemphera kuti adzamupemphelere mwana wawoyo. Koma M’busa Zambia anauza makolo a mtsikanayo kuti amutenga azikamupemphelera kunyumba kwake. Koma atapita kunyumbako, m’busayo amagona naye mpaka kumupatsa mimba.

Atawona kuti mtsikanayo ndi woyembekezera, m’busayo ananyengelera makolo ake kuti angomukwatira mwana wawoyo, zomwe sizinasangalatse makolowo ndipo anakanena ku polisi.

M’busa Zambia ndi wa m’mudzi wa Makaula mfumu yaikulu Mabuka m’boma lomwelo la Mulanje.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

SATCP advances infrastructure plans

MBC Online

BWALO LA MILANDU LABWEZA GALIMOTO YA UMBONI WABOMA

MBC Online

Akakhala ku ndende zaka 19 chifukwa chovulaza mkazi wake wakale

Charles Pensulo
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.