Anthu a midzi ya Mphampha ndi Tsambalabooka kwa mfumu yaikulu Lundu ku Chikwawa ati ndi okondwa kuti tsopano adzimwa madzi aukhondo.
Anthuwa anena izi kampani za Garda World ndi Illovo Sugar Malawi zitakhazikitsa madzi a m’mipopi m’midzi iwiriyi.
Paramount Chief Lundu ya m’derali yati anthu m’midziyi sadzidwalanso matenda otsekula m’mimba pafupifupi chifukwa tsopano adzimwa madzi aukhondo ndi otetezedwa.
Mayi Nalesi Fambauwone, a m’mudzi wa Mphampha, ati poyamba amadzuka m’bandakucha kukafunafuna madzi, zimene anati zimayika pachiopsezo chitetezo chawo.
Mkulu wa kampani ya Gardaworld, a Ganizani Kanchiputu, wati kampanizi zagwiritsa ntchito ndalama pafupifupi K122 million pokonza madziwo, amene apindulire anthu 2,000 m’midzi iwiriyi.