Bungwe la Malawi Communication Regulatory Authority (MACRA) lati laika ndalama zokwana K6 billion mu gawo loyamba la ntchito yomanga zipinda zophunzilira luso la makono musukulu 75 za m’dziko muno.
Mkulu wa bungweli, a Daud Suleman, anena izi pa bwalo la sukulu ya Msambachikho ku Lilongwe, imene ili mdera la Lilongwe City South, limene phungu wake ndi nduna yoona zakunja, a Nancy Tembo, pomwe amakhazikitsa ntchito yomanga chipindachi pa sukuluyi.
Iwo ati izi zithandiza kwambiri kukwaniritsa masomphenya a 2063, omwe cholinga chake n’kuonetsetsa kuti dziko lino ndi lodzidalira pa chuma komanso lotukukuka.
A Suleman ati ndikofunika kuti ana ndi achinyamata akhale ndi upangiri waluso la makono kuti apeze mayankho pa mavuto amene dziko lino likukumana nalo kaamba kakuti dziko la pansi likutukuka kwambiri m’magawo a lusoli.
Gawo lachiwiri la ntchitoyi liyamba m’mwezi wa June ndipo pofika chaka cha mawa akhala amaliza ntchitoyi, m’madera 193 a aphungu m’dziko lino.
Zipinda 75 ndi zomwe akuzimanga mugawo loyambali ndipo pofika m’mwezi wa September ophunzira akhala alowamo ndipo mwa zina, zipindazi zikhala zolumikizidwa ku makina a intaneti.