Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani Sports

Mabedi wavomereza kuti Flames ili mu gulu lovuta mu AFCON 2025

Mphunzitsi watimu yadziko lino yamasewero ampira wamiyendo ya Flames, Patrick Mabedi, wati gulu lomwe timuyi yapezekamo pofuna kudzigulira malo kumpikisano wa Africa Cup of Nations ndilovuta.

Malawi ili mu gulu L limodzi ndi matimu a Senegal,Burkina Faso komanso Burundi.

Mabedi wati timuyi ikuyenera kukonzekera mokwanira kuti idzachite bwino m’masewero amene aseweredwe miyezi ya September, October ndi November chaka chino.

Senegal ndiwo anali akatswiri a AFCON 2021  pomwe Burkina Faso yapezekamo kumpikisanowu kokwana ka 13.

 

Olemba: Praise Majawa

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MBC HONOURS CHUNGA FOR INITIATING ENTERTAINERS OF THE YEAR PROGRAMME

MBC Online

FAM ipepesa ku Goshen Trust

Emmanuel Chikonso

Salima Sugar makes K2.4 billion profit

Yamikani Simutowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.