Bungwe loyendetsa masewero a mpira wa manja m’dziko muno la NAM lati kukanika kuyendetsa bwino chuma kumasewerowa kukuthamangitsa kampani zimene zili ndi kuthekera kokweza masewerowa.
Mlembi wa mkulu wa bungweli, a Yamikani Kauma, ndi amene ayankhula izi munzinda wa Lilongwe pa maphunziro a zachuma amene anakonza ndi a Old Mutual, omwe amathandiza masewerowa m’chigawo chapakati kudzera ku kampani yawo yotchedwa MPICO.
A Patricia Chatsika, m’modzi mwa akuluakulu a ku Old Mutual, anati cholinga cha maphunzirowa ndi kuthandiza osewera komanso oyendetsa masewerowa m’mene angagwiritsire ntchito ndalama.
Osewera ndi oyendetsa masewero a Netball okwana 100 m’chigawo chapakati ndi amene achita nawo maphunzirowa.