Bungwe lothana ndi ziphuphu komanso katangale la ACB latsimikiza kuti lamanga anthu asanu ndi m’modzi powaganizira kuti amachita zachinyengo pa ntchito yodinda ziphaso ku nthambi ya Immigration.
Ofalitsankhani ku ACB, a Egrita Ndala, ati anthuwa awamanga kuti akayankhe mafunso okhudza m’chitidwe wa ziphuphu komanso katangale.
“Zoonadi tamanga anthuwa potsatira madandaulo a anthu komanso kafukufuku wachinsinsi yemwe tinachita okhudza zachinyengo kunthambiyi, ” anatero a Ndala.
Anayi mwa anthuwa ndi ogwira ntchito ku Immigration ndipo awiri enawo samagwira ntchito kumeneko.