Vuto lochedwa kubwezeretsa ndalama kwa munthu amene walakwitsa nambala pakati pa banki ndi foni, posachedwapa likhala mbiri yakale chifukwa ma banki ndi kampani za lamya za m’manja akambirana za m’mene angalithetsere.
Izi amakambirana lero masana pa msonkhano wa Bankers Association of Malawi (BAM) omwe ukuchitikira m’boma la Mangochi.
Nkhaniyi inayamba pamene mkulu wa kampani ya Airtel Malawi, a Charles Kamoto, amafotokozera ma membala a BAM kuti anthu ambiri amadandaula za kuchedwaku.
Iwo anayamikiranso ma Banki kaamba kothandiza kuti a Malawi ambiri adzifikiridwa ndi njira za makono zotumiza ndi kulandilira ndalama.