Nduna yoona zaulimi, a Sam Kawale lero ili nawo pamwambo umene wakonzedwa ndi alimi aku Lilongwe, amene asonkhanitsa ndalama zoposa K1.7 biliyoni zogulira zipangizo zaulimi.
Iyi ndi pologalamu yapadera yomwe inayamba ndigulu la alimi pa Extension Planning Area (EPA) ya Mitundu m’chaka cha 2009 ndipo pano inafalikira m’ma EPA 34 ndipo pano pali magulu alimi oposa 100.
Mwambowu ukuchitika pasukulu yapulaimale ya Phiri la Njuzi kwamfumu yaikulu Masumbankhunda m’boma la Lilongwe.
Mkulu wazaulimi ndi chilengedwe m’boma la Lilongwe, a Ezra Mbendera, ati ndalamayi agulira feteleza ndipo K700,000 ipita ku mbewu.
Mayi Joyce Sakasa, omwe ndi wapampando wanthambi za alimi m’bomali, ati akuika mtima paulimi ndi cholinga choti anthu adzikhala odzidalira pachuma ndi chakudya.