Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani Politics

Amayi atenge mbali pa ndale — MHRC

Bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lapempha nthambi zosiyanasiyana kuti zithandize amayi ndi kuwalimbikitsa kuti akwanitse kutenga nawo mbali pandale.

M’modzi wa akuluakulu ku MHRC, a Deborah Tambulasi Banda, ndi amene amayankhula izi pamkumano omwe anakonza ku Lilongwe ndi nthambi zosiyanasiyana pofuna kuwunikirana momwe angathanirane ndi mavuto omwe amayi amakumana nawo pa ndale.

“Tikufuna pakhale 50/50 maka pa udindo akuluakulu mundale kapena 60/40 chaka cha 2025 kupita kutsogolo,” anatero a Banda.

Wapampando wa komiti yoona zofalitsa uthenga ku nyumba ya malamulo, komanso phungu wa dera la kumadzulo kwa boma la Chikwawa, a Susan Dossi, anapempha amayi kuti azidzikhulupilira ndi kupewa kuponderezana komanso kudziyang’anira pansi pochita ndale.

Mkulu wa bungwe la Malawi Council of Disability Affairs (MACODA), a George Chiusiwa, anati ndi koyenera kuti aliyense adzitenga nawo gawo pa ndale kaamba kakuti ndi ufulu wa aliyense.

A Chiusiwa anatinso akukambirana ndi bungwe loyendetsa zisankho la MEC kuti awunikire malamulo ena omwe amapsinja anthu awulumali ngakhalenso amayi pandale.

 

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

MUST unveils ambitious six-year strategic plan

MBC Online

NTLEP hails media, clergy in fight against TB and Leprosy

MBC Online

Dr Usi ati alimbikitsa umodzi

Secret Segula
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.