Malawi Broadcasting Corporation
Local Local News Nkhani Sports Sports

‘Ku Ntchisi kuli luso lamasewero’

“Achinyamata ambiri m’boma la Ntchisi ali ndi luso lozama pa masewero,” awa ndi mawu amene ayankhula a Anderson Msonthi amene akuthandiza masewero a mpira wamiyendo ndi wamanja.

Iwo amayankhula izi Lamulungu atapereka zikho kwa amene apambana mpikisano wa Anderson Msonthi Football and Netball Trophies wa ndalama zokwana K5 Million ku mvuma kwa bomalo.

A Msonthi anati awonetsetsa kuti athandizire kutukula luso losiyanasiyana m’derali.

Timu ya mpira wa miyendo ya Mwinowa FC ndi timu ya mpira wa manja ya Malambo Sisters ndi amene akhala akatswiri a mu chikhochi atapikisana ndi matimu ena okwana 133 amene anatenga nawo gawo pa masewerowa kuyambira pa 23 December 2023.

Mwinowa FC yapambana itagonjetsa Mafuta FC ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi. Ndipo timu ya Malambo Sisters yagonjetsa Mwinowa Sisters ndi zigoli zisanu ndi zinayi kwa zinayi.

Matimu amene awapatsa mphoto za ndalama ndi amene athera poyambilira mpakana pachinayi ndipo timu iliyonse imene inatengapo gawo ikuyembekezeka kulandira mpira ngati mbali imodzi yotukula masewerowa.

Amene anapereka mphatsozi ndi akastwiri a mpira wa miyendo akale monga Fischer Kondowe, Chiwukepo Msowoya ndi Joseph Kamwendo.

Olemba: Yamikani Makanga

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FOOTBALL GETS ITS SHARE OF CHAKWERA’S TRIP

MBC Online

Commonwealth commends Malawi for its resilience

Kumbukani Phiri

NKHUDZI BAY WATER PROJECT IMPROVING COMMUNITIES’ LIVES

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.