Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Alimi musatengeke ndi mavenda – MUSCCO

Bungwe la Malawi Union of Savings and Credit Cooperatives (MUSCCO) lapempha alimi m’dziko muno kuti asagulitse mbewu zawo kwa ochita malonda osatsata ndondomeko ndi cholinga chiti apeze phindu lochuluka pa zokolola zawo.

A Fumbani Nyangulu omwe ndi mkulu wa MUSCCO, ayankhula izi m’boma la Dedza kumene iwo amayendera ntchito yopereka upangiri wabwino kwa alimi.

Ntchitoyi pa chingerezi akuyitcha kuti Community Economic Participation Enhancement Support to Farmer Organizations and Trade Associations.

M’modzi mwa alimi achitsanzo a Mark Phiri ati ndi kofunika kuti alimi ambiri awaphunzitse m’mene angasamalire ndalama zomwe amapeza akagulitsa zokolola zawo kaamba koti ambiri mwa iwo samasungitsa ndalama zawo m’mabumgwe osunga ndalama kapena ma banki.

Mark Phiri-Mwini Munda wa Chimanga

“Nafe timafuna titapindula ndi ndalama za zokolora koma ambirife mitu imasokonekera ndi mtengo wa mavenda omwe umakhalanso otibera,” a Phiri anafotokoza.

Bungwe la MUSCCO limapereka upangiri wa kasamalidwe ka ndalama ndipo likugwira ntchitoyi ndi alimi ndi thandizo la ndalama lochokera ku bungwe la m’dziko la Sweden la We Effect.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Kamang’aleni akakuchitirani nkhanza — Mfumu Mwamlowe

Rudovicko Nyirenda

‘Apatseni chisamaliro chabwino ana’

Olive Phiri

Achinyamata adziwe kufunika kolembetsa mkaundula wa voti – Mumba

Emmanuel Chikonso
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.