Bungwe la MACRA la limbikitsa a Malawi kuti adzikamang’ala ku Polisi ngati anthu ena awalakwira kapena kuwachitira upandu pa masamba a mchezo komanso malo ena pa makina a intaneti, mkulu wa bungweli a Daudi Suleiman anatsimikiza.
Mkulu wa Nthambi ya Computer Emergency Response Team (CERT) ku MACRA, a Christopher Banda, ati izi zikudza pamene madando akuchuluka okhudza anthu amene amachita malonda komanso kuwonetsa luso lawo pa makinawa kuti a Polisi sakumathandiza mokwanira powateteza, zomwe zikuchititsa kuti ntchito yawo isapite patsogolo.
Mwa maupandu ena, ndi monga kutsegula ma accaount abodza pa masamba a mchezo ndi cholinga chofuna kuna,iza, kunyoza komanso kubera ndalama anthu osadziwa.
Olemba : Yamikani Makanga