Malawi Broadcasting Corporation
Development Local Local News Nkhani

Kafukufuku wati kulorena kwakula m’boma la Mangochi

Kafukufuku oona mmene anthu a m’boma la Mangochi akuchitira pa ntchito yolimbikitsa kukhala mololerana komanso mwa mtendere waonetsa kuti khalidwe lochitirana zamtopola likuchepa.

Professor Kennedy Machila akusukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (LUANAR) ndi amene anachita kafukufukuyi limodzi ndi bungwe la Centre For Social Concern limene lakhala likugwira ntchito yophunzitsa adindo osiyanasiyana m’bomali za ubwino okhala mololerana.

Poyankhula pamene amapereka zotsatira zakafukufukuyi, a Professor Machila anati “m’mbuyomu boma la Mangochi limadziwika ndi mikangano yamipingo, koma pano Asilamu ndi Akhristu akukhala limodzi molemekeza zikhulupiliro za aliyense”.

Komabe, iwo anapempha khonsolo ya bomali kuti ilembe ntchito munthu yemwe adzilandira nkhani zokhudza kusiyana maganizo zomwe zingamafike ku ofesi ya Bwanamkubwa kuti adzitha kulondoleza bwino lomwe chifukwa nkhani zina zimatsala m’mitima mwa anthu chifukwa chosaoneka mmene zathela.

Yemwe anayimira Bwanamkubwa wa bomali, a Venus Juma, anati khonsoloyi ichita chilichonse chotheka kuti mikangano ichepe m’boma la Mangochi maka pamene dziko lino likukonzekera chisankho cha chikulu m’mwezi wa September.

“Ndondomeko tili nazo zomwe timayesetsa kuti anthu a ndale adzitsata kuti pasakhale mikangano koma ndi momwe taonera zotsatira zakafukufukuyi tipezanso njira zatsopano kuti ntchito yokhazikitsa mtendere ikhale ya tanthauzo,” a Juma anatero.

Mwa zina, bungwe la Centre for Social Concern limagwiritsa ntchito mipikisano ya masewero a mpira komanso mikumano yosiyana siyana ngati njira yobweretsera anthu pamodzi ndi kuwaphunzitsa zakufunikira kokhala mololerana.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Mabedi waitananso Gaba

Romeo Umali

Allocate more funds to NEEF — CSO

Timothy Kateta

UK-based Malawian striker making strides

Romeo Umali
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.