A Jacqueline Bokosi omwe ndi eni ake a kampani ya Chisurija Transport Services (CTS) alangiza amayi komanso achinyamata m’dziko muno kuti azivomereza ndi kupita chitsogolo akagweredwa mavuto monga kusowa ntchito ndi kutaya okondedwa awo.
A Bokosi amayankhula izi mu mnzinda wa Lilongwe pa msika wa Nsungwi ku Area 25 pamene amakhazikitsa malo atsopano a kampani yawo, imene imalandira ndi kutumiza katundu.
Iwo anati zinali zovuta kupitiliza kuyendetsa kampaniyi chifukwa amuna awo, a Richard Bokosi, anamwalira ndipo anazindikira kuti sangasinthe chifuniro cha Mulungu koma kuvomereza basi.
Padakali pano, CTS yakwanitsa kulemba ntchito achinyamata ndi amayi okwana 68 ndipo ili ndi nthambi 17 m’zigawo zonse za dziko lino ndipo ntchito ili mkati yofuna kutsegula nthambi zina m’madera omwe kulibe.