Malawi Broadcasting Corporation
Nkhani

Gwiritsani ntchito zitukuko kuti dziko lino lipindule

Nduna yoona za ubale wa dziko lino ndi maiko ena yemwenso ndi phungu wa dera la Lilongwe City South West a Nancy Tembo wapempha makolo ndi adindo a m’madera kuti akhale patsogolo kulimbikitsa ana pa ma phunziro ncholinga choti chitukuko chomwe ntchito boma likukhazikitsa mugawo la maphunziro chipinduliredi dziko lino.

Ndunayi yanena izi pa sukulu ya Msambachikho mdera lake pomwe limodzi ndi bungwe la MACRA amakhazikitsa ntchito yomanga chipinda chophunzilira luso la makono.

A Tembo ati mtsogoleri wa dziko lino wakhala akuchita nawo misonkhano yosiyanasiyana mmaiko kupezera dziko lino thandizo ndipo zipinda zomwe bungwe la MACRA likumangazi ndi chimodzi mwa zotsatira zake.

Sukulu ya Msambachikho ndi sukulu yokhayo ya pulayimale mwa sukulu 75 zomwe bungwe la MACRA ikumangamo zipindazi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

Bambo wafa atapsya ndi moto wa petrol

Emmanuel Chikonso

A Nankhumwa akhazikitsa chipani

MBC Online

A Kasambara awayika m’manda pa mwambo wachisilikali

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.