Malawi Broadcasting Corporation
Local Nkhani

Chakwera alembetsa mu kaundula wa voti

Mtsogoleri wa dziko lino, Dr Lazarus Chakwera komanso mayi wa dziko lino Madam Monica Chakwera, alembetsa mu kaundula wa voti pa sukulu  ya Malembo  m’boma la Lilongwe.

Dr Chakwera ndi mai wa dziko linoyu alembetsa mu kaundulayu pomwe akuchititsa misonkhano yoimaima yomemeza anthu kuti alembetse mkaundulayu m’boma la Lilongwe.

Atalembetsa mu kaundulayu, Mtsogoleri wa dziko linoyu walimbikitsa a Malawi onse kuti atengelepo chitsanzo pokalembetsa mu kaundulayu poti ati ndi ufulu wawo ndipo  akatelo zidzawapatsa mphamvu  yodzaponya voti    pa chisankho cha chaka cha mawa.

Bungwe la MEC linatsegulira gawo lachitatu  lolembetsa mu kaundulayu  lomwenso ndi lomaliza  28 November ndipo lidzatha pa 11 December.

Related posts

Boma, asodzi agwirana manja pofuna kuchulukitsa nsomba m’nyanja ya Malawi

Romeo Umali

President Dr Chakwera meets religious leaders

Romeo Umali

DODMA, UNDP push for disaster resilience

Rabson Kondowe
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.