Mwambo wa misa ya maliro a malemu bambo Claude Boucher Chagomerana Chisale watha pabwalo la Kungoni m’boma la Dedza.
Poyankhula, nduna yoona za malo, a Deus Gumba, anati mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi okhudzidwa kwambiri ndi imfa ya bambo Claude Boucher Chisale.
A Gumba ati dziko la Malawi lataya munthu yemwe anali odzipeleka pa ntchito yotumikira Mulungu komanso amalimbikitsa kuti chikhalidwe ndi chipembedzo zidziyendera limodzi komanso kusamalira za chilengedwe.
Monsignor Henry Chinkanda, a Diocese ya Dedza, ati malemu Boucher Chisale amaliza ulendo wawo bwino chifukwa cha ntchito zomwe anagwira ali ndi moyo pomwe anadzichepetsa ndi kukhala ngati m’Malawi wina aliyense ngakhale anali ochokera m’dziko la Canada.
A Chinkanda anayamikira malemuwa chifukwa cholimbikitsa chikhalidwe cha a Yao, a Ngoni ndi a Chewa.
A Chisale amwalira Lolemba pa chipatala cha Kamuzu munzinda wa Lilongwe.
A Chisale adabadwa pa 2 August m’chaka cha 1941 mu mzinda wa Montreal m’dziko la Canada ndipo anafika m’dziko muno pa 8 December m’chaka cha 1967.