Mmodzi mwa makhumutcha ochita malonda kwa Ngabu m’boma la Chikwawa Saeed Dinyelo lero wakhazikitsa chikho cha mpira wa miyendo cha ndalama zokwana K10 million.
Mwambowu unachitikira pa bwalo Ngabu Community m’bomalo.
Mmawu ake, Dinyelo anati wachita izi pamene ali ndi masomphenya oti derali lidzatulutse timu yomwe idzasewerere mu TNM Super League mtsogolomu.
Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo mdziko muno la FAM, a Daud Mtanthiko ayamikira a Dinyelo pothandizira kupititsa patsogolo masewerowa mdziko muno.
Phungu wa chipani cha MCP wa delari a Illias Karim anali nawonso pa mwambowu
Matimu okwana 32 ndi omwe atenge nawo mbali mu mpikisanowu.
Pamasewero okhazikitsa chikhochi, timu ya Mapoliko yagonjetsa Chimpambana Red Tigers ndi zigoli zitatu kwa ziwiri.
Olemba Nobert Jameson