Aphungu a nyumba ya malamulo a kukambirana ganizo lokhazikitsa lamulo lomwe livomereze ulimi wa chamba chakwathu kuno.
Phungu wa dera la kumwera kwa boma la Lilongwe Peter Dimba ndiyemwe wabweretsa ganizolo nyumbayi. Ena mwa maganizo amene aphungu apereka pothilira ndemanga paganizoli mnyumbayi ndikuti
lamulo lovomereza ulimiwu lidzakhale lokomera alimi achimalawi kuti ambiri adzakhale ndi mwayi opeza phindu lochuluka komaso kupereka mwayi wa ntchito.
Aphunguwa ati, mwazina, ulimi wa chamba utha kuthandiza dziko lino kupeza ndalama zakunja zochuluka.
Ndipo Mtsogoleri wa zokambirana mnyumbayi, a Richard Chimwendo Banda, ati ulimiwu ndi wabwino koma ndikofunika kuti amalawi aphunzitsidwe zokhudza ulimiwu poopa kubweretsa mavuto pakati pa achinyamata.
Padakali pano, aphunguwa akupitiriza kupereka maganizo awo pa nkhaniyi.