Apolisi m’boma la Mangochi amanga anthu anayi amene akuwaganizira kuti anathyola ndi kuba zakumwa zaukali zandalama pafupifupi K2.3 million pa malo ena ogulitsira mowa otchedwa ‘Pa Soko’.
Ofalitsankhani pa Polisi ya Mangochi, a Amina Tepani Daudi, anati mowa wina obedwa wapezeka ndipo mabotolo ena apezeka opanda kanthu.
“Mwini wake wa malowa anatidziwitsa kuti usiku wapa 8 September anatseka malowo cha m’ma 1 koloko m’mawa, koma kunja kutayera anazindikira kuti malowo anathyoledwa ndi anthu aupandu komanso anaba ndalama zokwana K120,000,” a Daudi anatero.
Anthu amene akuwaganizirawa ndi a Bongani Kachingwe, 26, Vincent Makhiringa, 32, Maxwell Shafi, 20 komanso Mkwanda Shahid, 22 ndipo akaonekera kubwalo lamilandu kuti akayankhe mulandu otchola nyumba ndi kuba katundu.