Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera ndi Madam Monica Chakwera ali ku Abu Dhabi m’dziko la United Arab Emirates (UAE) kumene achite zokambirana ndi mtsogoleri wa dzikolo, Sheikh Mohammed Bin Zayed Alhyan, pankhani zothandiza kuthetsa vuto lakusowa kwa mafuta agalimoto m’dziko muno.
Dr Chakwera afikira pa bwalo la ndege la Al Bateen Executive ndipo analandiridwa ndi kazembe wa dziko la Malawi m’dziko la Kuwait komanso akuluakulu a boma la UAE.
Sheikh Alhyan ndi amene anayitana Dr Chakwera kuti achite zokambiranazi.
Dziko la UAE ndi limodzi mwa mayiko amene chuma chawo chinakwera kwambiri kaamba kodalira ntchito zoyenga mafuta, zokopa alendo komanso ulimi wa minda ikuluikulu.
Olemba: Jackson Sichali, Abu Dhabi, UAE