Sukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources yati anthu mdziko muno asiye kuika patsogolo nsima ngati chakudya chokhacho koma kuti adzitha kudyaso zakudya zina.
Mphunzitsi pasukulu ya ukachenjede ya LUANAR, a Alexander Kalimbira anena izi pamsokhano otseka zokambilana zokhudza ulimi pakati pa adindo amchigawo cha kumwera kwa Africa.
A Kalimbira anati kukhala ndi chakudya chokwanila sikutanthauza kukhala ndi chakudya chambiri koma kukhalanso ndi chakudya choyenera zomwe anati a Malawi sakuyenera kudalira nsima yokha ngati dziko lino likufuna kuthana ndi vuto lokhala ndi chakudya chosakwanira.
Ndipo wapampando wa bungwe la CISANET, a Herbert Chagona ati msonkhanowu wakhala opindulitsa kudziko lino ponena kuti adindo akambirana zochuluka zofunikira pokweza miyoyo ya anthu mdziko muno kuphatikizapo kuwunikira malamulo osiyanasiyana okhudza ulimi ndi madyedwe abwino.