Oyimba Nyimbo za Uzimu Evance Meleka, watulutsa nyimbo imene ikukhuza imfa ya oyimba odziwika bwino Katelele Ching’oma.
Nyimbo-yi yomwe ikudziwika kuti “Bwanji Simunanene?” Muli uthenga odandaula za kumwalira kwa oyimba ena monga Atoth Manje ndi Thomas Chibade.
Ching’oma wamwalira dzulo ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe atangodwala kwa nthawi yochepa.
Pangodutsa miyezi Iwiri ndi sabata ziwiri zokha pamene oyimba onsewa atsikira kuli chete.
Olemba : Romeo Umali.