Malawi Broadcasting Corporation
Local Local Nkhani

Bungwe la MEC layamba kuonkhetsera zotsatira za chisankho kumsonkhano waukulu wachipani cha DPP

Akuluakulu a bungwe loona zachisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) ayamba ntchito yoonkhetsera ma voti omwe   nthumwi   ku msonkhano waukulu wachipani cha DPP zaponya.

Nthumwi za chipani cha DPP zili ku msonkhano waukulu omwe ukuchitikira ku Holo ya COMESA mu mzinda wa Blantyre. Nthumwizi zimaponya voti posankha akuluakulu achipanichi kuti akhale mmaudindo osiyanasiyana (National Governing Council) pokonzekera chisankho cha chaka cha mawa.

Nthumwi 2491 ndizimene zaponya voti, malinga ndi mmodzi mwa akuluakuku ku bungwe loona za chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), a Hastings Bota.

Mtsogoleri wa chipanichi,  a Peter Mutharika,  awavomereza kale kukhala odzaimira  chipanichi pa chisankho cha prezidenti chaka cha mawa.

Malinga ndi wapampando wa komiti yoyendetsa chisankhochi, Dr George Chaponda, pali anthu ena asanu ndi anai omwe alibe opikisana nawo pa maudindo kaamba koti panalibe anthu omwe anasonyeza chidwi pamaudindowo.

A George Chaponda omwe ndi wachiwiri kwa prezidenti wa DPP mchigawo cha  kum’mwera akupikisana ndi a Joseph Mwanamvekha pa udindowu.

A Bright Msaka akupikisana ndi a Loney Phiri pa udindo wa wachiwiri kwa prezidenti wa chipanichi mchigawo cha kum’mawa, pamene mchigawo cha pakati, a Alfred Gangata ndi a Paul Gadama akupikisana pa udindo wa wachiwiri kwa prezidenti mchigawochi.

Pa mpando wa mlembi wamkulu wachipanichi akupikisana ndi a Peter Mukhitho ndi a Clement Mwale.

A Mary Navicha ndi a Roza mbilizi akupikisana pa udindo wa mkulu wa amai m’chipani cha DPP, pamene a Gladys Ganda ndi a Jean Namathanga akupikisana pa udindo wa mkulu oona za chisankho mchipanichi.

A Chimwemwe Chipungu akupikisana ndi a Sameer Suleman pa mpando wa mlembi okonza zochitikachitika m’chipanichi.

Amene amayenera kupikisana ndi a Shadreck Namalomba pa udindo wa ofalitsa nkhani za chipani cha DPP a Gilbert Phiri Goliati ati sapikisana nawo paudindowu.

Ena mwa anthu omwe alibe opikisana nawo ndi a Jappie Mhango, pa mpando wa wachiwiri kwa prezidenti wa DPP mchigawo cha kumpoto, a Edgar Tembo alibe opikisana nawo pa mpando wa msungichuma wamkulu, pamene a Chifundo Makande alibe opikisana nawo ngati mkulu oona zokopa anthu komanso a Symon Vuwa Kaunda alibe opikisana nawo ngati mkulu oona za madongosolo ena mchipanichi (Director of logistics.)

Pali chiyembekezo choti bungwe la MEC lero lilengeza zotsatira za chisankhochi.

Print Friendly, PDF & Email

Related posts

FEDOMA commends government on support towards the disabled

Eunice Ndhlovu

MAGU She-Wolves defend Mo626 title

Yamikani Simutowe

SCIENCE BACKS SMOKE-FREE PRODUCTS

MBC Online
error: All Content is protected. Copyright © 2022. Malawi Broadcasting Corporation. All Right Reserved.